Langwan Piksy
Langwan Piksy - Kuzizira lyrics
Your rating:
Kukumazizira kukada Tsiku kuchedwa kutha kukacha Tsiku lonse mvula mawawa Sindingachedwe ndidziwe za mawa Mano anga anthu sawaona Sikweni kweni kusekelera Usiku zindivuta kugona Ngati udzudzu ndimachezera Moyo wathu dzana unkakoma Kachikondi kutsekemera Ubwino opanda mwina ‘pena koma Kachikondi kulemelera CHORUS Alipo akukukonda? Alipo akukuhoda? Alipo akukugwira? Ndikungoganizira eya Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah VERSE TWO Chikondi chinali on point Ngati nyimbo yolondola ma note Chinali perfect chinalibe fault Anthu wokamba ankati tiri hot Zoti chikondi chimawawa inali mphekesera Anthu ena akamakamba tinkangomvetsera Anthu akaduka kusowa chotigwetsera Koma lero tandiona ndingo fwenthera Maso anga ayandama in tears Mtima wanga udzadza ndi fear Usaganize zoti undisiye Ndikungoganizira CHORUS Alipo akukukonda? Alipo akukuhoda? Alipo akukugwira? Ndikungoganizira eya Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah VERSE THREE Kodi chikondi nnakupatsa chija nchokwanira? Kuti udzadikira mpaka nthawi idzakwanira? Ngakhale moto utawotcha udzakakamira? Chikondi chako chikuthawa kodi udzambwandira? Ndiwe wekha ndikufuna mdziko langa dear Mtima wako usakayike ndiwe wanga dziwa Ndi pemphero langa nthawi zonse ukumbukira Ndi kwa iwe kokha komwe mtima wanga ugundira CHORUS Alipo akukukonda? Alipo akukuhoda? Alipo akukugwira? Ndikungoganizira eya Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah